51 Zimenezi zinali zigawo za cholowa chimene wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni ndi atsogoleri a mafuko a Isiraeli anagawira anthu.+ Anagawa dzikolo pochita maere ku Silo+ pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.+ Choncho anamaliza kugawa dzikolo.