-
Numeri 32:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 ‘Amuna amene anatuluka mu Iguputo kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, sadzaliona dziko+ limene ndinalumbira kuti ndidzapereka kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo,+ chifukwa sanandimvere ndi mtima wonse. 12 Koma Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi, ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, adzaliona dzikolo chifukwa akhala akumvera Yehova ndi mtima wonse.’+
-
-
Deuteronomo 1:35, 36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 ‘Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa anthu a mʼbadwo woipa uwu amene adzaone dziko labwino limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu,+ 36 kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune. Iyeyu adzaliona, ndipo ndidzapereka dziko limene anafikako kwa iye ndi ana ake, chifukwa chakuti watsatira Yehova ndi mtima wonse.+
-