5 Kuyambira lero ana awiri amene unabereka ku Iguputo kuno ine ndisanabwere, akhala anga.+ Efuraimu ndi Manase akhala ana anga ngati mmene alili Rubeni ndi Simiyoni.+
16Gawo limene ana a Yosefe+ anapatsidwa+ linayambira kumtsinje wa Yorodano kufupi ndi Yeriko kukafika kumadzi akumʼmawa kwa Yeriko, kudutsa kuchipululu chochokera ku Yeriko kukafika kudera lamapiri la Beteli.+