23 Mʼdengu la mikate yosafufumitsa limene lili pamaso pa Yehova utengemo mkate wobulungira, mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta ndi mkate wopyapyala. 24 Zonsezi uziike mʼmanja mwa Aroni ndi mʼmanja mwa ana ake, ndipo uziyendetse uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova.