-
Numeri 2:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Asilikali onse a gulu la Rubeni amene analembedwa mayina alipo 151,450. Amenewa azikhala achiwiri kunyamuka.+
17 Posamutsa chihema chokumanako,+ gulu la Alevi lizikhala pakati pa magulu enawo.
Dongosolo limene azitsatira posamuka,+ ndi limenenso azitsatira pomanga misasa yawo, aliyense pamalo ake, mogwirizana ndi gulu lawo la mafuko atatu.
-