-
Deuteronomo 1:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
1 Awa ndi mawu amene Mose analankhula ndi Aisiraeli onse mʼchipululu, mʼchigawo cha Yorodano, mʼchigwa chimene chinali moyangʼanizana ndi Sufu, pakati pa Parana, Tofeli, Labani, Hazeroti ndi Dizahabi. 2 Kuchokera ku Horebe kupita ku Kadesi-barinea+ kudzera njira yakuphiri la Seiri pali mtunda woyenda masiku 11.
-