-
Numeri 14:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Komabe anthu onse amene aona ulemerero wanga ndi zizindikiro zanga+ zimene ndinachita ku Iguputo, komanso zimene ndachita mʼchipululu, koma apitiriza kundiyesa+ maulendo 10 onsewa, ndipo sanamvere mawu anga,+ 23 sadzaliona mʼpangʼono pomwe dziko limene ndinalumbirira makolo awo. Ndithudi, onse amene sakundipatsa ulemu, sadzaliona dzikolo.+
-