3 Nʼchifukwa chiyani Yehova watibweretsa kudziko lino kuti tidzaphedwe ndi lupanga?+ Akazi athu ndi ana athu adzatengedwa ndi adani.+ Kodi si bwino kuti tingobwerera ku Iguputo?”+
39 Komanso ana anu amene munanena kuti adzagwidwa ndi adani,+ ana anu amene lero sakudziwa chabwino kapena choipa, amenewa ndi amene adzalowe mʼdzikolo ndipo ndidzawapatsa dzikolo kuti likhale lawo.+