Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 22:5, 6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Iye anatumiza anthu kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori+ pafupi ndi Mtsinje* wamʼdziko lawo. Anawatuma kuti akamuitane kuti: “Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo aja afika kuno. Iwo adzaza dziko lonse lapansi+ kumene munthu angayangʼane, ndipo akukhala pafupi penipeni ndi dziko langa. 6 Tsopano tabwerani chonde, mudzatemberere anthuwa+ chifukwa ndi amphamvu kuposa ineyo. Mwina ndingawagonjetse nʼkuwathamangitsa mʼdziko lino, chifukwa ndikudziwa kuti munthu amene inu mwamudalitsa, amakhaladi wodalitsika, ndipo munthu amene mwamutemberera, amakhaladi wotembereredwa.”

  • Numeri 23:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kenako Balamu ananena ndakatulo yakuti:+

      “Balaki mfumu ya Mowabu wandibweretsa kuno kuchokera ku Aramu,+

      Kuchokera kumapiri akumʼmawa kuti:

      ‘Bwera, udzanditembererere Yakobo.

      Bwera, udzaitanire tsoka pa Isiraeli.’+

  • Numeri 23:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Kenako Balaki anauza Balamu kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandichitira zimenezi? Ndakubweretsani kuno kuti mudzatemberere adani anga, koma inu mwawadalitsa.”+

  • Numeri 24:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kenako Balaki anapsera mtima Balamu. Ndiyeno Balaki anawomba mʼmanja mokwiya nʼkuuza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere adani anga,+ koma iwe wawadalitsa kwambiri maulendo atatu onsewa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena