-
Numeri 22:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Balamu anayankha Mulungu woonayo kuti: “Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu ndi amene watumiza anthuwa kuti adzandiuze kuti, 11 ‘Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo aja adzaza dziko lonse lapansi kumene munthu angayangʼane. Tsopano bwerani, mudzatemberere anthuwa.+ Mwina ndingathe kumenyana nawo nʼkuwathamangitsa.’”
-
-
Nehemiya 13:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Pa tsiku limenelo buku la Mose linawerengedwa anthu onse akumva.+ Iwo anapeza kuti mʼbukumo analembamo kuti mbadwa iliyonse ya Amoni ndi ya Mowabu+ isamaloledwe kukhala mʼgulu la anthu a Mulungu woona,+ 2 chifukwa iwowa sanapatse Aisiraeli chakudya ndi madzi. Mʼmalomwake, analemba ganyu Balamu kuti awatemberere.+ Koma Mulungu wathu anasintha temberero limenelo kukhala dalitso.+
-