44 Mʼmasiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa.+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa anthu a mtundu wina uliwonse.+ Koma udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa+ ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.+
15 Mngelo wa 7 analiza lipenga lake.+ Ndiyeno kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana akunena mokweza kuti: “Ufumu wa dziko wakhala Ufumu wa Ambuye wathu+ ndi wa Khristu wake+ ndipo iye adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale.”+