Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “‘Musapange milungu yopanda pake,+ chifaniziro,+ kapena chipilala chopatulika kuti muzichilambira. Musaike mwala wogoba+ mʼdziko lanu kuti muziugwadira,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.

  • Deuteronomo 4:15, 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mukhale tcheru,* chifukwa pa tsiku limene Yehova analankhula nanu kuchokera pakati pa moto ku Horebe, simunaone kalikonse mʼmotowo. 16 Choncho musamale kuti musachite zinthu mosakhulupirika popanga chifaniziro chilichonse chosema, chifaniziro cha chinthu chilichonse chachimuna kapena chachikazi,+

  • Deuteronomo 4:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Samalani kuti musaiwale pangano la Yehova Mulungu wanu limene anachita ndi inu+ ndipo musapange chifaniziro chosema, chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu anakuletsani.+

  • Deuteronomo 27:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 ‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wopanga chifaniziro chosema+ kapena chifaniziro chachitsulo+ nʼkuchibisa.* Chifanizirocho, chomwe ndi ntchito ya manja a mmisiri waluso,* ndi chonyansa kwa Yehova.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’*)

  • Machitidwe 17:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Choncho, popeza ndife ana a Mulungu,+ tisaganize kuti Mulunguyo ali ngati golide, siliva, mwala kapena chilichonse chosemedwa ndi anthu aluso.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena