Levitiko 19:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Komanso, musamakolole mphesa zotsala zamʼmunda mwanu kapena kutola mphesa zimene zamwazika mʼmunda mwanu. Zimenezo muzisiyira anthu osauka*+ ndi mlendo wokhala pakati panu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Deuteronomo 24:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Musamabere mwachinyengo waganyu yemwe ndi wovutika ndiponso wosauka, kaya akhale mmodzi wa abale anu kapena mlendo amene akukhala mʼdziko lanu, amene ali mʼmizinda yanu.*+ Salimo 146:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Yehova akuteteza alendo amene akukhala mʼdziko la eni.Amathandiza mwana wamasiye komanso mkazi wamasiye.+Koma amasokoneza mapulani a anthu oipa.*+
10 Komanso, musamakolole mphesa zotsala zamʼmunda mwanu kapena kutola mphesa zimene zamwazika mʼmunda mwanu. Zimenezo muzisiyira anthu osauka*+ ndi mlendo wokhala pakati panu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
14 Musamabere mwachinyengo waganyu yemwe ndi wovutika ndiponso wosauka, kaya akhale mmodzi wa abale anu kapena mlendo amene akukhala mʼdziko lanu, amene ali mʼmizinda yanu.*+
9 Yehova akuteteza alendo amene akukhala mʼdziko la eni.Amathandiza mwana wamasiye komanso mkazi wamasiye.+Koma amasokoneza mapulani a anthu oipa.*+