Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 12:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Musamalambire Yehova Mulungu wanu mwa njira imeneyi, chifukwa iwo amachitira milungu yawo zinthu zonse zonyansa zimene Yehova amadana nazo. Iwo amafika ngakhale powotcha ana awo aamuna ndi aakazi pamoto kuti ikhale nsembe kwa milungu yawo.+

  • 2 Mafumu 16:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ahazi+ mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anakhala mfumu mʼchaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya.

  • 2 Mafumu 16:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Anayenda mʼnjira ya mafumu a Isiraeli+ ndipo anafika mpaka potentha* pamoto mwana wake wamwamuna,+ potsatira zinthu zonyansa zimene anthu a mitundu ina ankachita+ amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa Aisiraeli.

  • 2 Mbiri 28:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Ahazi+ anakhala mfumu ali ndi zaka 20 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Davide kholo lake.+

  • 2 Mbiri 28:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Kuwonjezera pamenepo, Ahazi anapereka nsembe yautsi mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu.* Iye anawotcha ana ake pamoto+ potsatira zinthu zonyansa zimene ankachita anthu a mitundu ina+ amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa Aisiraeli.

  • Salimo 106:35-37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Koma anayamba kusakanikirana ndi anthu a mitundu ina,+

      Nʼkuyamba* kuchita zinthu ngati mmene iwo ankachitira.+

      36 Ankatumikira mafano awo,+

      Ndipo mafanowo anakhala msampha kwa iwo.+

      37 Ankapereka nsembe ana awo aamuna

      Komanso ana awo aakazi kwa ziwanda.+

  • Yeremiya 32:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kuwonjezera pamenepo, anamangira Baala malo okwera mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu*+ kuti aziwotcha* ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto ngati nsembe kwa Moleki.+ Ine sindinawalamule+ kuti azichita zimenezi. Ndipo sindinaganizirepo mumtima mwanga* zowauza kuti achite chinthu chonyansa chimenechi, chimene chachititsa kuti Yuda achimwe.’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena