11 Choncho Aisiraeli anayamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova ndipo anayamba kutumikira Abaala.+ 12 Iwo anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa mʼdziko la Iguputo+ nʼkuyamba kutsatira milungu ya anthu owazungulira.+ Anayamba kugwadira milunguyo ndipo anakhumudwitsa Yehova.+