Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 49:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, mpaka Silo* atabwera.+ Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+

  • Numeri 24:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndidzamuona, koma osati panopa;

      Ndidzamupenya, koma osati posachedwa.

      Nyenyezi+ idzatuluka mwa Yakobo,

      Ndodo yachifumu+ idzatuluka mu Isiraeli.+

      Ndipo iye adzaphwanyadi chipumi cha Mowabu+

      Ndi mitu ya asilikali onse ankhanza.

  • Luka 7:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ataona zimenezi anthu onse anachita mantha ndipo anayamba kutamanda Mulungu kuti: “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu.”+ Ananenanso kuti, “Mulungu wakumbukira anthu ake.”+

  • Yohane 1:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Kenako Filipo anakumana ndi Natanayeli+ nʼkumuuza kuti: “Ife tapeza Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti. Chilamulo cha Mose komanso zimene aneneri analemba zimanena za iyeyu.”

  • Yohane 6:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Anthuwo ataona chizindikiro chimene anachitacho, anayamba kunena kuti: “Mosakayika uyu ndi mneneri uja amene anati adzabwera padziko.”+

  • Machitidwe 3:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ndipotu Mose ananena kuti, ‘Yehova* Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine kuchokera pakati pa abale anu.+ Mudzamumvere pa zinthu zonse zimene adzakuuzeni.+

  • Machitidwe 7:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Ameneyu ndi Mose amene anauza Aisiraeli kuti, ‘Mulungu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati pa abale anu.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena