-
Deuteronomo 3:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi kukafika kuchigwa cha Arinoni,* ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a Aamoni. 17 Ndinawapatsanso Araba, mtsinje wa Yorodano ndi malo amʼmbali mwa mtsinjewo, kuchokera ku Kinereti* mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere* imene ili mʼmunsi mwa zitunda za Pisiga, chakumʼmawa.+
-