8 Atachoka kumeneko anapita ku Penueli ndipo anawapemphanso chimodzimodzi, koma amuna a ku Penueli anamuyankha ngati mmene amuna a ku Sukoti aja anamuyankhira. 9 Choncho anauzanso amuna a ku Penueli kuti: “Ndikabwerako bwino, nsanja yanuyi ndidzaigwetsa.”+