-
1 Mbiri 18:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Davide anagonjetsa Hadadezeri+ mfumu ya Zoba+ pafupi ndi Hamati,+ pamene Hadadezeriyo ankapita kukakhazikitsa ulamuliro wake kumtsinje wa Firate.+ 4 Davide analanda Hadadezeri magaleta 1,000 komanso anagwira amuna 7,000 okwera pamahatchi ndi asilikali 20,000 oyenda pansi.+ Kenako Davide anapundula* mahatchi onse a magaleta nʼkungosiya mahatchi 100.+
-