-
1 Mbiri 19:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Patapita nthawi, Aamoni anaona kuti akhala ngati chinthu chonunkha kwa Davide. Choncho Hanuni ndi Aamoni anatumiza anthu nʼkuwapatsira matalente* asiliva 1,000 kuti akabwereke magaleta komanso kulemba ganyu asilikali okwera pamahatchi a ku Mesopotamiya,* a ku Aramu-maaka ndi a ku Zoba.+ 7 Choncho anakabwereka magaleta 32,000 ndiponso kulemba ganyu mfumu ya ku Maaka ndi anthu ake. Zitatero, iwo anabwera nʼkumanga misasa yawo pafupi ndi Medeba.+ Aamoni anatuluka mʼmizinda yawo nʼkusonkhana kuti akamenye nkhondo.
-