-
2 Samueli 10:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasonkhanitsa Aisiraeli onse nʼkuwoloka Yorodano kupita ku Helamu. Ndiyeno Asiriya anayalana kuti akumane ndi Davide ndipo anayamba kumenyana naye.+ 18 Koma Asiriyawo anayamba kuthawa Isiraeli ndipo Davide anapha asilikali a Siriya 700 okwera magaleta komanso asilikali 40,000 okwera pamahatchi. Iye anaphanso Sobaki, mtsogoleri wa gulu lankhondo la Siriya.+ 19 Mafumu onse amene anali atumiki a Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisiraeli, nthawi yomweyo anakhazikitsa mtendere ndi Aisiraeli nʼkuyamba kuwatumikira.+ Asiriya anachita mantha kwambiri moti sanayesenso kuthandiza Aamoni.
-