-
1 Mbiri 27:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka 20 kutsika mʼmunsi, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisiraeli ngati nyenyezi zakumwamba.+ 24 Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga anthu koma sanamalize. Ndipo Mulungu anakwiyira kwambiri Aisiraeli chifukwa chowerenga anthuwo,+ moti chiwerengerocho sichinalembedwe mʼmbiri ya zochitika za nthawi ya Mfumu Davide.
-