Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 30:12-16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Ukamachita kalembera wa ana a Isiraeli,+ aliyense azipereka dipo la moyo wake kwa Yehova pa nthawi imene ukuwawerengayo. Azichita zimenezi kuti mliri usawagwere pochita kalemberayo. 13 Anthu onse amene awerengedwa azipereka zinthu izi: hafu ya sekeli* yofanana ndi sekeli yakumalo oyera.*+ Magera* 20 amakwana sekeli imodzi. Hafu ya sekeli ndi chopereka kwa Yehova.+ 14 Aliyense amene wawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita mʼtsogolo azipereka chopereka kwa Yehova.+ 15 Mukamapereka kwa Yehova chopereka chophimba machimo kuti muwombole moyo wanu, anthu olemera asapereke zochuluka, ndipo osauka asapereke zosakwana hafu ya sekeli.* 16 Uzilandira ndalama zasiliva zophimbira machimo kwa Aisiraeli nʼkuzipereka kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wapachihema chokumanako. Ndalama zimenezi zidzathandiza kuti Yehova azikumbukira Aisiraeli komanso zidzaphimba machimo anu kuti muwombole moyo wanu.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena