11 Alevi akanyamula bokosilo nʼkupita nalo kwa mfumu ndipo akaona kuti muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mtumiki wa wansembe wamkulu ankabwera nʼkukhuthula ndalamazo.+ Kenako ankabwezeretsa bokosilo pamalo ake. Ankachita zimenezi tsiku ndi tsiku moti anasonkhetsa ndalama zambiri.