-
Numeri 9:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Munthu aliyense pakati panu kapena pakati pa mbadwa zanu, amene wadetsedwa chifukwa chokhudza mtembo,+ kapena amene ali pa ulendo wautali, azikonzabe nsembe ya Pasika yopereka kwa Yehova. 11 Azikonza nsembeyo mʼmwezi wachiwiri+ pa tsiku la 14, madzulo kuli kachisisira.* Azidya nyama ya nsembeyo pamodzi ndi mikate yopanda zofufumitsa, ndiponso masamba owawa.+
-