24 “Lankhula ndi Aisiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Mʼmwezi wa 7, pa tsiku loyamba la mweziwo, muzipuma pa ntchito zanu zonse. Limeneli ndi tsiku la chikumbutso, ndipo lipenga likalira+ muzisonkhana kuti mulambire Mulungu.
27 “Tsiku la 10 mʼmwezi wa 7 umenewu, ndi Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo.+ Muzichita msonkhano wopatulika ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni*+ chifukwa cha machimo anu ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova.