-
Levitiko 16:29, 30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Mʼmwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo, muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni* chifukwa cha machimo anu ndipo aliyense wa inu asamagwire ntchito ina iliyonse,+ kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale. 30 Pa tsiku limeneli machimo anu adzaphimbidwa+ kuti muyesedwe oyera. Mudzakhala oyeretsedwa ku machimo anu onse pamaso pa Yehova.+
-