-
Levitiko 23:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 “Tsiku la 10 mʼmwezi wa 7 umenewu, ndi Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo.+ Muzichita msonkhano wopatulika ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni*+ chifukwa cha machimo anu ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. 28 Pa tsiku limeneli musamagwire ntchito iliyonse, chifukwa ndi tsiku lochita mwambo wophimba machimo+ anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
-