-
Aheberi 9:24-26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Khristu sanalowe mʼmalo oyera opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Panopa iye ali kumwamba kuti azionekera pamaso pa Mulungu mʼmalo mwa ifeyo.+ 25 Iye sanapite kumwambako kuti azikadzipereka nsembe mobwerezabwereza, ngati mmene mkulu wa ansembe amachitira. Paja mkulu wa ansembe amalowa mʼmalo oyera chaka ndi chaka+ atatenga magazi a nyama, osati ake. 26 Zikanatero, akanavutika mobwerezabwereza kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa. Koma tsopano iye waonekera kamodzi kokha pamapeto a nthawi* ino kuti achotse uchimo kudzera mu nsembe yake.+
-