10 Aroni azipaka ena mwa magazi a nyama ya nsembe yamachimo panyanga za guwalo kuti aphimbe machimo+ a nyangazo. Azichita zimenezi kamodzi pa chaka+ mʼmibadwo yanu yonse. Kwa Yehova guwalo ndi lopatulika koposa.”
7 Koma mʼchipinda chachiwiricho, mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankalowamo kamodzi pa chaka,+ ndipo sankalowa popanda kutenga magazi.+ Magaziwo ankawapereka chifukwa cha iyeyo,+ komanso chifukwa cha machimo a anthu+ amene anawachita mosadziwa.