-
Levitiko 16:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Akatero azituluka nʼkupita kuguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova kuti akaliphimbire machimo. Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ngʼombe yamphongo ndi a mbuzi nʼkuwapaka panyanga zonse za guwa lansembe. 19 Ena mwa magaziwo aziwadonthezera paguwalo ndi chala chake maulendo 7, kuti likhale lopatulika komanso kuti aliyeretse ku zinthu zodetsa za Aisiraeli.
-