-
Levitiko 23:27-31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 “Tsiku la 10 mʼmwezi wa 7 umenewu, ndi Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo.+ Muzichita msonkhano wopatulika ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni*+ chifukwa cha machimo anu ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. 28 Pa tsiku limeneli musamagwire ntchito iliyonse, chifukwa ndi tsiku lochita mwambo wophimba machimo+ anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29 Munthu aliyense amene sadzasonyeza kuti akudzimvera chisoni* chifukwa cha machimo ake pa tsiku limeneli adzaphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+ 30 Munthu aliyense wogwira ntchito iliyonse pa tsiku limeneli, ndidzamuwononga nʼkumuchotsa pakati pa anthu a mtundu wake. 31 Musamagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale ku mibadwo yanu yonse, kulikonse kumene mungakhale.
-