-
Levitiko 25:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Koma mʼchaka cha 7 dzikolo lizidzasunga sabata lopuma pa zonse, sabata la Yehova. Musamadzadzale mbewu mʼminda yanu kapena kudulira mitengo yanu ya mpesa. 5 Musamadzakolole mbewu zomera zokha kuchokera pa mbewu zimene munakolola chaka chapita, ndipo musamadzakololenso mphesa za mʼmitengo yanu yosadulirayo. Chaka chimenecho dziko lizidzapuma pa zonse.
-