-
Ekisodo 29:40, 41Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Popereka mwana wa nkhosa woyamba, uzipereka limodzi ndi ufa wosalala, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* wothira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini,* ndi gawo limodzi mwa magawo 4 a vinyo wa nsembe yachakumwa. 41 Uzipereka mwana wa nkhosa wachiwiri madzulo kuli kachisisira.* Uzimupereka pamodzi ndi nsembe yambewu komanso nsembe yachakumwa ngati mmene unachitira mʼmawa. Uzipereke kuti zikhale kafungo kosangalatsa,* nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.
-