13 Ndi ndani amene anayezapo mzimu wa Yehova,
Ndipo ndi ndani amene angamulangize ngati mlangizi wake?+
14 Kodi anafunsirapo nzeru kwa ndani kuti amuthandize kumvetsa zinthu?
Ndi ndani amene amamuphunzitsa njira yachilungamo,
Kapena kumuphunzitsa kuti adziwe zinthu,
Kapenanso kumusonyeza njira yokhalira womvetsadi zinthu?+