15 Koma mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu poonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mudzatembereredwa ndipo zinthu zoipa zotsatirazi zidzakuchitikirani:+
16 Mudzakhala otembereredwa mumzinda komanso mudzakhala otembereredwa mʼmunda.+