-
Yoswa 7:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anatenga Akani+ mwana wa Zera, limodzi ndi siliva uja, chovala chamtengo wapatali chija, mtanda wa golide uja,+ komanso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu, nkhosa, ndiponso hema wake, ndi chilichonse chomwe chinali chake, nʼkupita nawo kuchigwa cha Akori.+ 25 Ndiyeno Yoswa anati: “Nʼchifukwa chiyani watibweretsera tsoka?*+ Lero Yehova akubweretsera iweyo tsoka.” Atatero, Aisiraeli onse anayamba kuwaponya miyala+ anthuwo ndipo kenako anawatentha ndi moto.+ Umu ndi mmene anawaphera, anawaponya miyala.
-
-
Esitere 9:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Izi zinali choncho chifukwa Hamani+ mwana wa Hamedata, mbadwa ya Agagi,+ amene ankadana ndi Ayuda onse, anawakonzera Ayudawo chiwembu kuti awaphe.+ Ndiponso iye anachita Puri+ kapena kuti maere, nʼcholinga choti awasokoneze maganizo nʼkuwapha. 25 Koma Esitere atakaonekera kwa mfumu, mfumuyo inalemba+ lamulo lakuti: “Chiwembu chimene anakonzera Ayuda+ chimubwerere iyeyo.” Choncho Hamani komanso ana ake anawapachika pamtengo.+
-