10 Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu,+
Kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.+
11 Mofanana ndi mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi,
Chikondi chokhulupirika chimene amasonyeza anthu amene amamuopa ndi chachikulu kwambiri.+
12 Mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa,
Mulungu waikanso zolakwa zathu kutali ndi ife.+