Salimo 40:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Masoka amene andizungulira ndi ambiri moti sindingathe kuwawerenga.+ Zolakwa zanga ndi zochuluka moti sindikutha kuona kumene ndikulowera.+Zachuluka kwambiri kuposa tsitsi lakumutu kwanga,Ndipo ndataya mtima. Aroma 7:23, 24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 koma ndimaona lamulo lina mʼthupi* langa likumenyana ndi malamulo amʼmaganizo mwanga+ nʼkundichititsa kukhala kapolo wa lamulo la uchimo+ limene lili mʼthupi* langa. 24 Munthu womvetsa chisoni ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likundichititsa kuti ndifeli? Agalatiya 5:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Chifukwa zimene thupi limalakalaka zimalimbana ndi mzimu ndipo mzimu nawonso umalimbana ndi thupi. Zinthu ziwiri zimenezi zimatsutsana kuti musachite zinthu zimene mumafuna kuchita.+
12 Masoka amene andizungulira ndi ambiri moti sindingathe kuwawerenga.+ Zolakwa zanga ndi zochuluka moti sindikutha kuona kumene ndikulowera.+Zachuluka kwambiri kuposa tsitsi lakumutu kwanga,Ndipo ndataya mtima.
23 koma ndimaona lamulo lina mʼthupi* langa likumenyana ndi malamulo amʼmaganizo mwanga+ nʼkundichititsa kukhala kapolo wa lamulo la uchimo+ limene lili mʼthupi* langa. 24 Munthu womvetsa chisoni ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likundichititsa kuti ndifeli?
17 Chifukwa zimene thupi limalakalaka zimalimbana ndi mzimu ndipo mzimu nawonso umalimbana ndi thupi. Zinthu ziwiri zimenezi zimatsutsana kuti musachite zinthu zimene mumafuna kuchita.+