18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbadwa* zako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+
21 Solomo ankalamulira maufumu onse kuyambira ku Mtsinje*+ mpaka kudziko la Afilisiti nʼkukafika kumalire ndi Iguputo. Maufumuwa ankabweretsa msonkho kwa Solomo komanso kumutumikira kwa moyo wake wonse.+