-
Ekisodo 18:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Pakati pa anthuwa, usankhepo amuna oyenerera,+ oopa Mulungu, okhulupirika, odana ndi kupeza phindu mwachinyengo.+ Amenewa uwaike kuti akhale atsogoleri a anthuwa, ndipo pakhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.+ 22 Pakakhala mlandu uliwonse atsogoleri amenewa aziweruza anthuwo. Mlandu ukakhala wovuta azibwera nawo kwa iwe,+ koma mlandu uliwonse waungʼono, aziweruza. Uwalole amunawa kuti azikuthandiza kuchita zimenezi, kuti udzichepetsere ntchito.+
-