Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 7:12-15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ukadzamwalira+ nʼkugona mʼmanda ndi makolo ako, ndidzachititsa kuti mbadwa* yako, mwana wako weniweni, akhale mfumu ndipo ndidzachititsa kuti ufumu wake ukhazikike.+ 13 Iye ndi amene adzamangire dzina langa nyumba,+ ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+ 14 Ine ndidzakhala bambo ake ndipo iye adzakhala mwana wanga.+ Akalakwitsa zinthu zina, ine ndidzamudzudzula ndi ndodo ya anthu ndi zikoti za ana a anthu.*+ 15 Ndipo chikondi changa chokhulupirika sichidzachoka pa iye ngati mmene ndinachichotsera pa Sauli,+ amene ndinamʼchotsa pamaso pako.

  • Salimo 132:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yehova walumbira kwa Davide.

      Ndithudi sadzalephera kukwaniritsa mawu ake akuti:

      “Ndidzaika pampando wako wachifumu

      Mmodzi wa ana ako.*+

  • Yesaya 55:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Tcherani khutu lanu ndipo mubwere kwa ine.+

      Mverani ndipo mudzapitiriza kukhala ndi moyo,

      Ndithu ine ndidzachita nanu pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale+

      Lokhudza chikondi chokhulupirika chimene ndinalonjeza Davide. Lonjezo limeneli ndi lodalirika.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena