-
1 Mafumu 8:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, mukwaniritse lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a mʼbanja lako sadzasiya kukhala pampando wachifumu wa Isiraeli. Chofunika nʼchakuti ana ako asamale mayendedwe awo poyenda mokhulupirika mʼnjira zanga ngati mmene iwe wachitira.’+
-
-
Yesaya 9:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ulamuliro* wake udzafika kutali
Ndipo mtendere sudzatha,+
Pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake
Kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndiponso kukhala wolimba
Pogwiritsa ntchito chilungamo+ ndiponso mtima wowongoka,+
Kuyambira panopa mpaka kalekale.
Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.
-
-
Yeremiya 33:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 “Yehova wanena kuti, ‘Ngati anthu inu mungathe kuphwanya pangano langa loti kukhale masana ndi pangano langa loti kukhale usiku, kuti masana ndi usiku zisafike pa nthawi yake,+ 21 ndiye kuti inenso ndingathe kuphwanya pangano langa ndi Davide mtumiki wanga+ kuti asakhale ndi mwana woti adzalamulire monga mfumu pampando wake wachifumu wa Davide.+ Ndingachitenso chimodzimodzi ndi pangano langa ndi atumiki anga Alevi omwe ndi ansembe.+
-
-
Machitidwe 13:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Atamuchotsa ameneyu, anawapatsa Davide kuti akhale mfumu yawo.+ Iyeyu Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Jese,+ munthu wapamtima panga.+ Ameneyu adzachita zonse zimene ndikufuna.’ 23 Mogwirizana ndi lonjezo lake, kuchokera pa mbadwa* za munthu ameneyu, Mulungu wabweretsa mpulumutsi mu Isiraeli, amene ndi Yesu.+
-