2 Samueli 7:16, 17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhalapobe mpaka kalekale. Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.”’”+ 17 Natani anauza Davide mawu onsewa ndiponso masomphenya onse amene anaona.+ Salimo 72:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Dzina lake likhalebe mpaka kalekale,+Ndipo lipitirize kutchuka kwa nthawi zonse pamene dzuwa lidzakhalepo. Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.+Mitundu yonse ya anthu imutchule kuti ndi wosangalala. Yesaya 11:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Nthambi+ idzaphuka pachitsa cha Jese,+Ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzabereka zipatso. Yeremiya 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzaike mfumu yolungama pampando wachifumu yochokera mʼbanja lachifumu la Davide.*+ Mfumuyo idzalamulira mʼdzikoli+ ndipo idzachita zinthu mwanzeru, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Yohane 12:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Ndiyeno gulu la anthulo linamuyankha kuti: “Ife tinamva mʼChilamulo kuti Khristu adzakhala kosatha.+ Nanga inu mukunena bwanji kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa mʼmwamba?+ Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndi ndani?” Chivumbulutso 22:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 ‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kuti adzachitire umboni zinthu zimenezi kwa iwe kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu komanso mbadwa ya Davide.+ Ndinenso nthanda yowala kwambiri.’”+
16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhalapobe mpaka kalekale. Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.”’”+ 17 Natani anauza Davide mawu onsewa ndiponso masomphenya onse amene anaona.+
17 Dzina lake likhalebe mpaka kalekale,+Ndipo lipitirize kutchuka kwa nthawi zonse pamene dzuwa lidzakhalepo. Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.+Mitundu yonse ya anthu imutchule kuti ndi wosangalala.
5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzaike mfumu yolungama pampando wachifumu yochokera mʼbanja lachifumu la Davide.*+ Mfumuyo idzalamulira mʼdzikoli+ ndipo idzachita zinthu mwanzeru, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+
34 Ndiyeno gulu la anthulo linamuyankha kuti: “Ife tinamva mʼChilamulo kuti Khristu adzakhala kosatha.+ Nanga inu mukunena bwanji kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa mʼmwamba?+ Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndi ndani?”
16 ‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kuti adzachitire umboni zinthu zimenezi kwa iwe kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu komanso mbadwa ya Davide.+ Ndinenso nthanda yowala kwambiri.’”+