Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 11:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nthambi+ idzaphuka pachitsa cha Jese,+

      Ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzabereka zipatso.

  • Yesaya 11:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pa tsiku limenelo muzu wa Jese+ udzaimirira ngati chizindikiro kwa anthu.+

      Anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awapatse malangizo,*+

      Ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.

  • Yesaya 53:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pawinawake* ndiponso ngati muzu wotuluka mʼnthaka youma.

      Saoneka ngati munthu wapadera kapena waulemerero,+

      Ndipo tikamuona, maonekedwe ake si ochititsa chidwi moti ife nʼkukopeka naye.*

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzaike mfumu yolungama pampando wachifumu yochokera mʼbanja lachifumu la Davide.*+ Mfumuyo idzalamulira mʼdzikoli+ ndipo idzachita zinthu mwanzeru, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

  • Yeremiya 33:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 ‘Mʼmasiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo ndidzameretsera Davide mphukira+ yolungama* ndipo mphukirayo idzaweruza mwachilungamo mʼdzikoli.+

  • Chivumbulutso 5:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Koma mmodzi wa akulu aja anandiuza kuti: “Tonthola. Taona! Mkango wa fuko la Yuda,+ muzu+ wa Davide,+ anapambana pankhondo+ moti ndi woyenera kumatula zidindo 7 zimene amatira mpukutuwo nʼkuutsegula.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena