-
Yoswa 23:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Tsopano limbani mtima kwambiri kuti muzitsatira zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la Chilamulo+ cha Mose, ndipo musapite kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 7 Ndiponso muzipewa kugwirizana* ndi mitundu+ imene yatsala pakati panu. Musamatchule nʼkomwe mayina a milungu yawo+ kapena kulumbira pa milunguyo, ndipo musamaitumikire kapena kuigwadira.+
-