-
Machitidwe 13:34-37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Ndipo mfundo yakuti iye anamuukitsa ndipo sangabwererenso kuthupi limene limavunda,* anaifotokoza chonchi: ‘Ine ndidzakusonyezani anthu inu chikondi chokhulupirika chimene ndinalonjeza Davide. Lonjezo limeneli ndi lodalirika.’+ 35 Ndipo salimo lina limanenanso kuti, ‘Simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.’+ 36 Davide anachita chifuniro cha Mulungu pa nthawi ya mʼbadwo wake, anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda a makolo ake ndipo thupi lake linavunda.+ 37 Koma amene Mulungu anamuukitsa uja thupi lake silinavunde.+
-