-
Ezekieli 1:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Ndinaona chinachake chowala ngati siliva wosakanikirana ndi golide,+ chimene chinkaoneka ngati moto umene ukuyaka kuchokera pa chimene chinkaoneka ngati chiuno chake kupita mʼmwamba. Komanso kuchokera mʼchiuno chake kupita mʼmunsi, ndinaona chinachake chooneka ngati moto.+ Pamalo onse omuzungulira panali powala 28 ngati utawaleza+ umene ukuoneka mumtambo pa tsiku la mvula. Umu ndi mmene kuwala kozungulira pamalopo kunkaonekera. Kunkaoneka ngati ulemerero wa Yehova.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi. Kenako ndinayamba kumva mawu a winawake akulankhula.
-
-
Danieli 7:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Ndinapitiriza kuyangʼana mpaka pamene mipando yachifumu inaikidwa ndipo Wamasiku Ambiri+ anakhala pampando wake wachifumu.+ Zovala zake zinali zoyera kwambiri+ ndipo tsitsi lake linali looneka ngati ubweya wa nkhosa woyera. Mpando wake wachifumu unkaoneka ngati malawi a moto ndipo mawilo a mpandowo ankaoneka ngati moto umene ukuyaka.+
-