-
Deuteronomo 6:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Ndiyeno Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene analumbira kwa makolo anu Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzakupatsani,+ dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yabwino imene simunamange ndinu,+ 11 yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zosiyanasiyana zabwino zimene simunagwirire ntchito, zitsime zimene simunakumbe ndinu komanso minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale ndinu, ndiye mukakadya nʼkukhuta,+
-
-
Yoswa 5:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Tsiku lotsatira, iwo anayamba kudya zokolola za mʼdzikomo. Pa tsikuli anayamba kudya mikate yopanda zofufumitsa+ ndiponso tirigu wokazinga. 12 Mana analeka kugwa pa tsikuli, pamene Aisiraeli anadya zokolola za mʼdzikomo. Kuyambira pamenepo, sipankakhalanso mana oti Aisiraeli azidya.+ Choncho chaka chimenechi nʼchimene iwo anayamba kudya zokolola za mʼdziko la Kanani.+
-