2 Nʼchifukwa chiyani anthu inu mukuwononga ndalama polipirira zinthu zimene si chakudya,
Ndipo nʼchifukwa chiyani mukuwononga ndalama zimene mwapeza polipirira zinthu zimene nʼzosakhutitsa?
Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino,+
Ndipo mudzasangalala kwambiri ndi zakudya zabwino.+